Khwimbi la anthu lasonkhana pa Parish ya Mua ku Mtakataka m’boma la Dedza komwe kuli mwambo wapachaka wa Kungoni Arts and Culture Festival.
Ku mwambowu kuli zochitika zosiyanasiyana kuphatikizapo mwambo wa mapemphero, magule a chikhalidwe komanso gulu loyimba nyimbo zachikhalidwe lochokera mdziko la Uganda la Br Jolly Joe Jazz Band.
Mwambowu womwe umachitika kamodzi pachaka umatsogoleredwa ndi akuluakulu a zipembedzo zosiyanasiyana komanso magulu a zachikhalidwe.
Chaka chino, mwambowu ukuchitika pamutu woti “Umwini ndiye maziko a dziko lathu, chimvano cha mavu choning’a pamimba”.