Mkulu wa bungwe lophunzitsa ntchito za luso la manja la Technical Entrepreneur and Vocational Education and Training Authoritiy (TEVETA), a Elwin Sichiola, alimbikitsa achinyamata amene adasiyira sukulu panjira kuti aphunzire ntchito za manja pofuna kukhala odziimira paokha.
A Sichiola anena izi pomwe amapereka katundu osiyanasiyana pamalo osungira ana amasiye ndi a chikulire a Chisomo Orphanage and Home for the Elderly kwa Nsundwe m’boma la Lilongwe.
Mkulu woyang’anira malowa, a Bernard Chikhasu, wayamikira bungwe la TEVETA ndipo anapemphanso ena akufuna kwabwino kuti awathandizeko ndi m’dadada oti ana ndi achikulire adzigonapo.
“Ambiri mwa anawa akugona mmakomo a anthu akufuna kwabwino kamba koti tilibe malo oti ana komanso achikulire atha kumausapo,” a Chikhasu atero.
Bungwe la TEVETA lapeleka katundu monga matilesi, sopo, ziwiya, sugar, feteleza ndi zina zambiri.