Kampani ya Sparc Systems yapereka K10 miliyoni yothandizira msonkhano omwe maiko osiyanasiyana amakambirana momwe angatukulire ndikumanga mizinda yapamwamba ndi yamakono.
Aka kakhala koyamba dziko la Malawi kuyendetsa msonkhanowu omwe uchitike ku Lilongwe pa kuchoka pa 17 kufika pa 19 October.
Polandira cheke chandalamazi, a Noel Kathako omwe ndimneneri wa msonkhanowu ati thandizoli lithandizira kusamalira anthu omwe adzabwere kumsonkhanowu.
M’modzi mwa akuluakulu ku Sparc Systems a Jessie Kambeye ati misonkhano yotereyi ndiyofunikira kwambiri kaamba koti imathandizira kupereka mlozo momwe dziko likuyenera kumangara mizinda yake yomwe ndiyamakono ndiyokomera mibadwo yomwe ikubwerayo.