Mkulu ofalitsankhani komanso kuyendetsa mipikisano ku bungwe la FAM, a Gomezgani Zakazaka, ati ntchito yofufuza ma passport a osewera atimu ya Flames omwe asowa m’dziko la Mali ikupitilirabe.
Malinga ndi malipoti, m’modzi mwa akuluakulu a timuyi anaiwala ma passport amenewa mu taxi yomwe anakwera.
Malawi ili m’dziko la Mali pomwe usiku uno ikuyembekezeka kuti isewele ndi timu ya Burkina Faso mu masewero a mu ndime yodzigulira malo ku mpikisano wa AFCON.
Kanema za MBC komanso wailesi ya Radio 2 fm zilengezera masewero wa omwe ayambe 9 koloko usiku uno.
Olemba: Amin Mussa