Bambo Maxmos Chipendo wazaka 66 wapempha khoti lina ku Zomba kuti limumvere chisoni ponena kuti ndiwachikulire koma khotilo lakana izi.
Bamboyo anapempha izi khotilo litamulamula kuti akakhale ku ndende zaka khumi ndizinayi 14 pa mlandu wogwililira mtsikana wazaka 14.
Mneneri wapolisi ku Zomba, Patricia Sipiliano, wati Chipendo anapita kwao kwa mtsikanayo kuti akafunsire maganyu komwe anapeza mtsikanayo ali yekhayekha.
Kenako Chipendo ananyengelera mtsikanayo ndikupita naye pa tchire lina lapafupi komwe anachita naye zosayenerazo.
Mchimwene wake wa mtsikanayo ndiye anamupezelera bamboyo ndipo anakanena kwa makolo ake omwe anakanena nkhaniyi ku polisi.
Ndipo kukhoti, bamboyo anapempha kuti amukhululukire popeza ndi wa chikulire ndipo sangakwanitse kukakhala kundende.
Koma woweruza milandu anaperekabe zaka khumi ndi zinayizo kuti ena omwe ali ndi maganizo oterowo asazachitenso.