Anthu atatu afa ndipo m’modzi akulandira thandizo la ku chipatala galimoto la mtundu wa Mazda Axela Hatchback litawagunda Lolemba m’mawa m’boma la Mangochi.
Ofalitsankhani wa polisi ya m’chigawo cha ku m’mawa, a Patrick Mussa, ati anthuwa anali pa mwambo wa chinamwali pa mudzi wa a Ndege pafupi ndi sitolo za pa Mpale kwa mfumu yayikulu Chimwala m’bomalo.
Atatuwa anavulala kwambiri m’mutu ndipo amwalira akulandira thandizo la mankhwala pa chipatala cha Ukalanga. Winayo wavulala kwambiri miyendo ndipo akulandira thandizo la mankhwala pa chipatala cha chikulu cha Mangochi.
A Mussa ati amene amayendetsa galimotoyo, a Frank Nguni, 29, anathawa ndi kusiya galimoto lawo pamalo angoziyo koma kenaka anakadzipereka yekha ku polisi.