Gulu lomwe likuzitcha ‘Mbadwa Zokhudzidwa’ lapempha anthu a ndale kuti asiye kugwiritsantchito imfa ya Dr Saulos Chilima pofuna kumema anthu kuti adziwakonda.
M’busa Thoko Banda, amene ndi m’modzi mwa akuluakulu a gululi amayankhula izi loweruka mu mnzinda wa Lilongwe ndipo anauza a Malawi kuti asiye kukhulupilira mabodza andale oterewa.
Mkulu winanso wa bungweli, a Billy Malata, anachenjeza a Malawi amene akufalitsa uthenga wabodza pa masamba a mchezo kuti azagamulidwa mlandu akawapeza.
A Malata analimbikitsanso chipani cha Malawi Congress (MCP) kuti chisachite ndale zonyoza.