Bungwe la Malawi Bureau of Standards (MBS) lati ndipofunika kuti zipatala za m’dziko muno zidzikhala ndi zipangizo zoyezera zosonyeza milingo kapena kulemera kwa zinthu komanso anthu.
Wachiwiri kwa mkulu wa bungweli, a Thomas Senganimalunje, ndi amene anena izi ku chipatala chachikulu cha Mzuzu Central pomwe bungweli limayesa zina mwa zipangizo zapa chipatalachi ngati zili zovomerezeka.
A Senganimalunje ati kuopsa kokhala ndi zipangizo zosayezedwa bwino za chipatala kumadzetsa mavuto monga kupereka makhwala osayenera kwa munthu, zomwe zingakhudze moyo wake.
“Tikugwira ntchitoyi m’zipatala zonse za m’dziko muno, kaya za mmadera aku midzi komanso m’matauni. Cholinga chathu ndikuonetsetsa kuti zipangizo monga masikelo zikupereka zotsatira zolondola zomwe zithandize kaperekedwe ka makhwala ndi thandizo losiyanasiyana kwa odwala,” atero a Senganimalunje
Ndipo ofalitsankhani za chipatala cha Mzuzu Central, Dr Arnold Kayira, anati kukhala ndi zipangizo zoyezedwa bwino ndi chiyambi chopereka thandizo loyenera kwa odwala.
Zina mwa zinthu zomwe aziyesa komanso kuzipatsa chilolezo cha mlingo ndi monga masikelo ndi zipangizo zoyezera kutentha kwa thupi, thermometers mchingerezi.
Bungwe la MBS likhala likugwira ntchito yowona zipangizozi kwa ulere m’zipatala za boma m’sabatayi ngati mbali imodzi yokumbukira tsiku loona za milingo pa dziko lonse lapansi, lomwe ndipa 20 May chaka chilichonse.
Olemba George Mkandawire