Woimba wachichepere Sife Mw, yemwe dzina lake lenileni ndi Silvia Sifenjanie Sande ndipo ali ndi zaka 21, wati nyimbo yake yatsopano ndi bvumbulutso loti litonthoze onse osweka mtima ndi mavuto osiyanasiyana monga nkhani zam’banja.
Iye wayankhula izi pamene wangotulutsa kumene kanema wa nyimbo yatsopanoyi yotchedwa ‘Make Melifa’.
Nyimboyi ikumadzafika pena poti ‘Make/Bambo a Melifa, chilichonse mukufuna mutha kutenga koma mtendere okha ndisiyireni’. Ikumafotokozanso za anthu amene banja likatha amabwereranso kudzasowetsa mtendere winayo ngakhale anayamba moyo wina.
“izi ndi nyimbo zomwe ambiri sitiyimba koma ndithu zili ndikuthekera kochilitsa onse osweka mtima. Anthu ayilandira bwino ndipo ayembekezere zazikulu kuchokera kwa ine,” Sife Mw.
Sife Mw amachokera ku Machinga kwa mfumu yaikulu Liwonde ndipo ndi mphunzitsi wakupulaimale pa sukulu ya Bolera m’boma la Mangochi.