Oyimba nyimbo zauzimu Steve Wazisomo Muliya wati nyimbo zotchyakuka bwino zitha kuthandiza kuchepetsa imfa za anthu amene amadzipha chifukwa cha nkhawa.
Muliya, amene anapambana chaka chatha mu mpikisano wa MBC Entertainers of the Year, wanena izi pamene watulutsa nyimbo yake yatsopano yotchedwa kuti Confidence imene wayimba ndi oyimba wina, Success.
Iye anati nyimboyi ndiyopereka chiyembekezo komanso chikhulupiliro kwa anthu amene ali ndi nkhawa.
“Ndizomvetsa chisoni kuti imfa za anthu amene akudzipha zikuchuluka, makamaka kwa anthu a amuna,” Muliya anatero.
Otsatira bwino nkhani zamsangulutso, a Herbert Katanda, anati nyimbo zokhala ngati zimenezi komanso masewero, mongotchula zochepa chabe, zimathandiza kutsuka nkhawa mu ubongo.
“Izi zili ndi kuthekera kopatsa anthu msangala, kupereka chiyembekezo komanso kulimbitsa mtima anthu,” a Katanda anatero.
M’mbuyomu, apolisi m’dziko muno analengeza kuti imfa za anthu odzipha zachuluka chaka chino kusiyana ndi chaka chatha.
Wachiwiri kwa ofalitsa nkhani za Polisi, a Harry Namwaza, anati kuyambira mu mwezi wa January mpakana June chaka chino, analandira malipoti kuti pachitika imfa 281 zamtunduwu, ndipo panambalayo, 246 anali abambo 35 okha anali amayi.
A Namwaza anati chaka chatha imfazi zinalipo 220 ndipo 198 zinakhudza abambo 22 zokha zinakhudza amayi.