Mkulu wa nthambi yoona zamaulendo apa ndege m’dziko muno (Department of Civil Aviation), a Vetrus Francis Dziwe, wati ntchito za maulendo apa ndege zikuyenda bwino popanda chilichonse chopinga.
Poyankhula ndi MBC Digital, a Dziwe ati apitiriza kuonetsetsa kuti zonse zili m’chimake.
“Ndege ya mammawa yopita ku Republic of South Africa yapita kalekale, apa anthu akukonzekera (ya 10 koloko) yopita ku Lusaka m’dziko la Zambia choncho palibe chopinga,” anatero a Dziwe.
Ndipo ena mwa akuluakulu aku nthambi yoona za anthu olowa ndi kutuluka m’dziko muno atsimikiza kuti malo onse anthambiyi, kuphatizapo mzipata zolowera mdziko muno, ntchito zikuyenda bwino lomwe.
Mmasamba amchezo mwakhala mukuzungulira kalata yokhala ngati kuti anthu ena ogwira ntchito ku Immigration amamema anzawo wogwira ntchito ku dipatimentiyi kuti lero Lachinayi pa 6 June ayambe kunyanyala ntchito zawo.
Ndipo chikalata china chikuonetsanso kuti unduna waza chitetezo cha m’dziko, omwe umayang’anira nthambiyi, wadzudzula mchitidwewu.
Malinga ndi chikalatacho, chomwe wasaina mlembi ku undunawu a Steven Kayuni, zomwe ma ofesalawo amafuna kuchita ndikulakwira malamulo kamba koti sadatsatire ndondomeko kukhala nthambi yaza chitetezo.