Katswiri oyimba amene amachokera m’boma la Phalombe, Giboh Pearson, wapulumuka pa ngozi ya galimoto yomwe wachita pomwe amapita ku phwando la msangulutso ku Bangwe mu mzinda wa Blantyre.
Malinga ndi Pearson, chiwongolero komanso mabuleki agalimoto lake zinasiya kugwira ntchito, zomwe zinachititsa kuti akanike kuwongolera galimotoli ndipo linatembenuzika.
“Ndachita ngozi koma ndili bwino,” watero Giboh patsamba lake la mchezo.
Pangoziyi palibe wavulala.