Bungwe la National Registration Bureau (NRB) lati linalemba anthu okwana pafupifupi 12.3 million chiyambireni ntchito yakalembera wa unzika m’chaka cha 2016.
Mkulu wa ntchito ya kalembera wa unzika ku NRB, a Mbawaka Mwakhwawa, ati pakati pa zaka za 2016 ndi 2023, NRB yalemba anthu pafupifupi 10.4 million, pamene kuchokera mwezi wa June chaka chatha kufikira mwezi wa June chaka chino, NRB yalemba anthu 1.6 million.
Poyankhula kwa olembankhani munzinda wa Lilongwe, a Mwakhwawa ati anthu oposa 350,000 ndi amene awalemba mu kaundula wa unzika wa dziko pa kalembera wapadera (Mop up exercise) yemwe bungweli likuchita.
“Tapereka ma certificate a anthu omwalira 600,000. Ndekuti padakali pano mu kaundula muli anthu 11.6 million,” a Mwakhwawa anatero.