Malawi Broadcasting Corporation
Local Local News Nkhani

NGORA yati K1BN ithandiza mabungwe awo kudzidalira

Mabungwe amene si aboma ayamikira boma poyika thumba lapadera la K1 bilion lothandiza ntchito za mabungwewa.

Mkulu wa bungwe la Non-Governmental Organisation Regulatory Authority (NGORA), a Edward Chileka-Banda, ayankhula izi pamkumano ophunzitsa mabungwe amene si aboma pankhani zokhudza thumbali munzinda wa Lilongwe.

Thumbali lithandiza mabungwewa kuti adzitha kugwira ntchito zawo mosatsamira kwambiri thandizo lakunja.

A Banda anadzudzula mabungwe ena kaamba kokanika kugwiritsa bwino ntchito ndalama, zimene anati zathamangitsa othandiza ena akunja.

M’modzi mwa akuluakulu ku unduna owona zachisamaliro cha anthu, a Geoffrey Chimwala, anati mabungwe makumi awiri amatsekedwa kaamba kamavuto azachuma, zimene anati pano zichepa.

“Awa ndi mabungwe omwe amathandiza kukwaniritsa ndondomeko zachitukuko zaboma kotero akuyenera kukhala odzidalira kuti ntchito zawo zipitilire,” a Chimwala anatero.

Mkulu wabungwe la Civil Society Education Coalition (CISEC), a Benedicto Kondowe, atsutsa zoti thumbali ndi lotseka pakamwa mabungwe omenyera ufulu wa anthu ponena kuti zimene boma lachita ndi zomwenso mayiko akunja amachita pothandiza ntchito zamabungwe omwe si aboma.

Ganizo lathumbali linabwera ndi mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, m’chaka cha 2023 poyankhula kumtundu wa aMalawi pofuna kuti mabungwewa athe kulimbana ndi umphawi ndi mavuto omwe nzika zimakumana nawo mmalo momangodikira mabungwe a mayiko akunja.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

The claimant was overpaid — AG

Austin Fukula

Malawi celebrates World Sight Day

MBC Online

Tembo finally gets his Lifetime Achiever Award

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.