Nduna yoona za maphunziro a ukachenjede, Jessie Kabwila, ati bungwe la Higher Education Students’ Loans and Grants Board (HESLGB) ndi lofunika kwambiri pokweza ntchito zamaphunziro m’dziko muno.
A Kabwila anena izi pamene akuyendera nthambi za boma komanso sukulu zimene zili pansi pa unduna wao.
Mwa zina, andunawa apempha bungwelo kuti lifikire anthu onse m’dziko muno pofuna kuonetsetsa kuti palibe kusiyana kwakukulu pakati pa anthu olemela ndi osauka.
“Ndi masomphenya a mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, kuti bungwe la HESLGB lidzilandira ndalama zochuluka kufikira ophunzira onse ovutika ndi cholinga chokwaniritsa masomphenya a Malawi 2063,” iwo anatero.
A Kabwila anati boma litengera bilo yokhudza zamaphunziro a ukachenjede ku nyumba ya malamulo ngati mbali imodzi yokweza maphunziro apamwamba m’dziko muno.
Mkulu wa bungwe la HESLGB, a Prince Phwetekere, ati aonetsetsa kuti akufikira ophunzira onse ovutika ndi ngongole za sukulu.
A Phwetekere anati akhazikitsa njira zothandiza kuonetsetsa kuti ophunzira amene amaliza maphunziro awo akubweza ngongole kuti ena athenso kupindula.