Malawi Broadcasting Corporation
Development Local Local News Nkhani Politics

Jiya wayamikira chitukuko, wadzudzula mchitidwe oononga

Phungu wadera la pakati munzinda wa Lilongwe wayamika boma kaamba ka ntchito zachitukuko zomwe likugwira mdera lawo.

Phunguyi, a Alfred Jiya, wati boma lawamangira misewu ndi milatho yomwe yathandiza ku nkhani ya mayendedwe.

Iwo atinso panopa boma likupaka phula msewu wa pakati pa Area 18 kukafika ku Area 50 koma anadzudzula mchitidwe wa anthu ena omwe akumaononga zitukukozi.

“Pali anthu ena awononga mlatho omwe unamangidwa pa mtsinje wa Nankhaka omwe umathandiza anthu akwa Mgona ndiku Area 27. Moyo umenewu ndi odana ndi chitukuko, tisaononge chitukuko,” anatero a Jiya.

Olemba: Isaac Jali

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Mbali ina ya msewu wa Chiwembe sanamange bwino — Chimwendo Banda

MBC Online

VANDALISM COST MALAWIANS ELECTRICITY

MBC Online

Madotolo okonza nkhope za anthu afika

Jeffrey Chinawa
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.