Apolisi ku Zomba amanga Frederick Masiku wazaka 46 ndi mkazi wake Fasilen Golosi wazaka 38 chifukwa chokaniza kutengera mwana wawo kuchipatala chifukwa cha chipembedzo.
Mneneri wapolisi ku Zomba Patricia Sipiliano wati mwana wa banjalo wazaka zisanu anadwala mutu. Kenako banjalo linayamba kupemphelera mwanayo koma mwatsoka anamwalira.
Banjali ndi la mmudzi wa Ramusi 2 Mfumu yaikulu Ramusi ku Zomba.