Membala watsopano wachipani cha Malawi Congress (MCP) a Uladi Mussa athokoza mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera chifukwa chokhulukira milandu yawo ndi ya mtsogoleli wakale wa dziko lino Dr Bakili Muluzi.
A Mussa kenako anamema anthu a m’boma la Machinga kuti alowe chipani cha MCP chifukwa ndiko kuli chitukuko.
Iwo amafotokoza izi pa msonkhano wa chitukuko omwe anachititsa ndi a Ken Zikhale Ng’oma m’boma lomweli komwe anauza mtundu wa a Malawi kuti amayenera kutuluka m’ndende pa 12 February, 2024.
Padakali pano, komiti yonse ya chipani cha Democratic Progressive (DPP) ya dera la Machinga East yatuluka chipanicho ndipo yalowa MCP.
Uyu ndi Kanema amene akuonetsa zina mwa zomwe zinali pa msonkhano umenewu.
#mbconlineservices