Phungu wanyumba ya malamulo wa dera la kumpoto chakummawa kwa boma la Machinga, Ajilu Kalitendere, walangiza anthu a m’dera lake kuti alandire ufa umene boma likugawa kutsatira njala imene yagwa m’dziko muno.
A Kalitendere amayankhula ku Nainunje kwa mfumu yaikulu Kapoloma ku Machinga kumene bungwe loona za ngozi zogwa mwadzidzidzi la DoDMA lagawa matumba a ufa okwana 1,254 kwa omwe akhudzidwa ndi njala.
Iye anauza anthuwo kuti akatengera zakuti MCP ndiyomwe ikugawa ufawo pomwe iwo ndi achipani china, afa ndi njala.
Wolemba: Davie Umar