Alimi a fodya m’dziko muno ati ndiosangalala ndi m’mene malonda a fodya ayambira pa msika.
President wa Tobacco Association of Malawi (TAMA) trust, a Abiel Kalima Banda, ati mitengo ya fodya ya chaka chino yaposa zaka zam’mbuyomu.
“Mitengo imeneyi ilimbikitsa alimi pa ulimi wawo,” atero a Kalima Banda.
Malonda a fodya ku Limbe ayamba pa mtengo wa 3 dollars 11 cents ndipo mtengo otsika ndi 2 dollars 20 cents.