Malawi Broadcasting Corporation
Development Local Local News Nkhani

Mfumu Mponela yakhutira ndi chitukuko cha msewu wa M1

Mfumu yaikulu Mponela yayamika mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera kaamba ka ntchito yokonzanso msewu wa M1 omwe udaonongeka kwambiri.

Inkosi Mponela yanena zimenezi pa Mtengowanthenga ku Dowa komwe Dr Chakwera ayima pa ulendo wawo opita ku chigawo chakumpoto kukagwira ntchito zosiyanasiyana.

Iwo ayamikiranso mtsogoleri wa dziko linoyu chifukwa cha masomphenya okonzanso njanji kuti sitima ziyambenso kuyenda, patapita zaka zoposa makumi awiri njanjiyo ili yoonongeka.

“Masomophenya anu ndi ofuna kutukula dziko lino ndipo ife mafumu aku Dowa tigwira nanu ntchito bwana,” anatero mfumu Mponela.

Phungu waderali, a Halima Daudi nawo ayamika boma kaamba koti ntchito yomanga zipatala zing’onozing’ono ili mkati, kuonjezera pa ntchito yokonza msewu wa M1.

Olemba: Isaac Jali

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Cancer cases still rising

MBC Online

‘Boma liteteze atsikana nthawi ya ngozi zadzidzidzi’

Emmanuel Chikonso

NYCOM hailed for youth agricultural empowerment

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.