Ofalitsa nkhani ku bungwe la Malawi Bureau of Standards (MBS), a Wazamazama Katatu, ati bungweli likutsegula sitolo zimene eni ake awaitana kuti akonza mavuto amene analipo.
A Katatu ati sitolozi aziunikanso ngati zakwaniritsa kufikira ndondomeko za ukhondo zimene bungweli limafuna.
Iwo ati sitolo zimene sizikwaniritsa malamulo a ukhondo ndi mfundo za bungweli zikhala chitsekere mpakana pamene atakonze mavutowa.
Mkulu wa sitolo ya Panda ku Area 49 mumzinda wa Lilongwe, a Aaron Mkwezalamba, anati iwo akonza mavuto onse amene analipo m’sitolo yawo monga kupenta komanso kuchotsa mafiliji oonongeka, mwa zina.
A Mkwezalamba ati kuyendera kwa bungwe la MBS mu sitolo yawo kwa waunikira zina zimene samadziwa ndipo ati aonetsetsa kuti akutsata malamulo a ukhondo a bungweli kupita chitsogolo.
Kufikila lero m’mawa, MBS yalandira pempho kuchokera kusitolo zinayi zomwe zinatsekedwa Lolemba kuti akaziyenderenso.