Ochita malonda (Mavenda) aku Nsungwi ku Area 25 mu mzinda wa Lilongwe atseka shop ya m’mwenye wina yemwe amadziwika bwino ndi dzina lakuti Farook ponena kuti wakhala akulowetsa malonda awo pansi.
Anthu okhudzidwa ati mkuluyu amatsitsa kwambiri mitengo ya katundu wawo.
A Albert Zuwawo, omwe amagulitsa zipangizo za katundu osiyanasiyana (Hardware) ati ndi povuta kuti alimbane ndi a Farook popeza iwo ali ndi mpamba ochepa.
“Pa chifukwa ichi, tatseka shopuyo kuti iye apite komwe kuli olimbana naye pa chuma ife za ziwawa ayi,” anatero a Zuwawo.

Wapampando wa msikawu, a John Mbumba, ati iwo amakanika kuti alowelerepo popeza m’mwenyeyo amawapatsa ndalama ngati yowatsekera pakamwa, yomwe ati imalowa ku thumba la msika komanso katundu wina amapanga yekha.
Mlembi wa ku unduna woona za malonda, a Christina Zakeyu, auza MBC Digital kuti padakali pano iwo adakafufuzabe za nkhaniyi.
Poyankhulapo, a Kate Kamwangala, omwe ndi mtsogoleri wa bungwe la Black Indigenous Business Network, ati ndi kofunika kuti ochita malonda a ang’ono adzikhala otetezedwa pofuna kuti athandize kukweza chuma cha dziko lino.
Msika wa Nsungwi anautsekula m’chaka cha 2002 mu mzinda wa Lilongwe.
#MBCDigital
#Manthu