Matupi ena a abale asanu ndi m’modzi (6) amene adatisiya pa ngozi ya ndege ku Chikangawa m’boma la Mzimba, anyamuka kupita ku maboma osiyanasiyana kuti akaikidwe n’manda.
Ma pulogalamu akuti a Lucas Kapheni ndi a Chisomo Chimaneni omwe amagwira ntchito ku Polisi akawaika lero ku Kasungu ndi ku Ntchisi ndipo ena akaikidwa mawa pa 14 June.
Ena akulowera ku Thyolo kumene kukayikidwe Major Flora Selemani Ngwinjili ndipo Colonel Owen Sambalopa akayikidwa ku Zomba ndipo Major Wales Aidini akayikidwa ku Mangochi pamene Daniel Kanyemba ayikidwa ku Lilongwe.
By Mirriam Kaliza
#MBCDigital
#Manthu