Mkulu wa ma Sheikh m’dziko muno, Grand Mufti Muhammad Uthman, wadandaula ndi mchitidwe othetsa mabanja m’dziko muno, ngakhalenso a chipembedzo cha chisilamu.
A Uthman anati, kudzera kubungwe la Islamic Information Bureau, akulandira madandaulo othetsa mabanja okwana 40 pa zana lililonse.
Iwo anati ambiri mwa iwo akumakhala achinyamata a zaka zakubadwa zapakati pa 20 ndi 35.
Iwo anati izi zili chomwechi kaamba kakuti achinyamata akumatsatira makhalidwe akunja komanso moyo otsanzira anzawo.
Chifukwa cha ichi, ofesi ya Grand Mufti of Malawi ndi Lilongwe City Centre Muslim Jamaat anayitanitsa msonkhano wa maphunziro okhudza za m’banja kwa mabanja achisalamu.