Masewero ndi njira yabwino yofalitsira mauthenga a uchembere wabwino komanso kudziwa za ma ufulu a achinyamata pa nkhani zogonana komanso banja, bungwe la Umunthu Foundation latero.
Mkulu wa bungweli, a David Odali, anena izi pa mkumano ndi achinyamata osewera mpira miyendo komanso wa manja ndi aphunzitsi a matimu 20 pa bwalo lamasewero a Mpira, ku Chiwembe mu mzinda wa Blantyre.
Iwo anati achinyamata amakonda kupezeka pa malo pamene pa kuchitika masewero, kotero pakufunika kuwagwiritsa ntchito pofalitsa mauthenga otere.
Pa mkumanowu, bungwe la Umunthu Foundation linaperekanso mipira ku matimuwa.