Bungwe lomwe limawona za mchitidwe ogwiritsa ntchito mankhwala osaloledwa mmasewero la Malawi Anti-Doping Organisation (MADO) lati kugwiritsa ntchito mankhwala oletsedwa mmasewero kuli ndikuthekera koipitsa mbiri yadziko.
Mlembi wa bungweli, a Leonard Sharra, anena izi mu mzinda wa Lilongwe pomwe bungweli likuphunzitsa atolankhani komanso atsogoleri ndi alembi anthambi zamasewero mdziko muno zokhudza momwe angathanirane ndi mchitidwewu.
“Ngati wina atayezedwa nkupezeka kuti amagwiritsa ntchito mankhwala kuti awonjezere mphamvu ndikupeza chipambano, zidzaononga mbiri yamasewero komanso dziko,” anatero a Sharra.
Mmawu ake mkulu owona zamasewero ku unduna wa zamasewero, a Jameson Ndalama, ayamikira MADO kaamba ka mamphunzirowa ndipo ati kuphwanya malamulo kukhala kusamvera chabe koma aphunzitsidwa zonse zoyenelera kutsatira pamasewero.
Malinga ndi wapampando wa MADO, a James Mwenda, bungweli lalandira ndalama zokwana pafupifupi $20,000 kuchokera ku komiti yoona za masewero pa dziko lapansi kuti zithandize kufalitsa uthenga okhudza kugwiritsa ntchito mankhwala ndi njira zosaloledwa mmasewero.