Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

A Malawi Mudzifunsa Mafunso Atsogoleri Anu Mmalo Momangodandaula — Usi

Nduna yoona za chilengedwe ndi kusintha kwa nyengo, Dr Michael Usi, yalangiza a Malawi kuti adzitha kumafunsa mafunso  atsogoleri awo mmalo momangodandaula akaona kuti zinthu sizikuyenda moyenera.

https://youtu.be/GXBmM9R_U7E

A Usi amayankhula ku Chirimba CCAP mu mzinda wa Blantyre pamene anali nawo pa mwambo wa mapemphero.

Iwo ati atsogoleri a mipingo akuyenera kulimbikitsa anthu kuti adzifunsa atsogoleri monga nduna za boma ndi aphungu, mwachitsanzo, chifukwa chimene kudera kwawo sakulandira ndalama za Mtukula Pakhomo, mwa zina.

Iwo atinso anthu adzifunsa aphungu awo momwe ndalama za chitukuko cha mmadera (CDF) azigwiritsira ntchito, poganizira kuti mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera anakweza CDF kuchoka pa K40 million kufika pa K100 million kuti chitukuko chidzioneka mmadera.

Wolemba: Arthur Chokhotho

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Apolisi agwira mbala zomwe zinaba katundu wa Radio Maria

Mayeso Chikhadzula

Bungwe la SFFRFM lati zokonzekera AIP zili m’chimake

Charles Pensulo

Ekhaya, Blue Eagles akwapulana la mulungu

Yamikani Simutowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.