Mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, wanyamuka m’chigawo chakummwera, kudzera pa bwalo la ndege la Chileka, kubwelera ku Lilongwe.
A Chakwera anali m’chigawo chakummwera pa Limbe Police Training School mumzinda wa Blantyre, kumene anatsogolera mwambo otulutsa apolisi omwe atsiriza maphunziro awo.
Nduna ya zofalitsa nkhani, a Moses Kunkuyu, nduna yoona za madzi ndi ukhondo, a Abida Mia, mafumu komanso atsogoleri andale ndi ena mwa anthu omwe anatsanzikana ndi Dr Chakwera komanso Madam Monica Chakwera pabwalo la ndege la Chileka.