Bwalo la milandu la First Grade m’boma la Mzimba lalamula a Emmanuel Khowaya,32, kuti akagwire ukayidi wa kalavula gaga kwa zaka khumi ndi ziwiri atawapeza olakwa pa mlandu ogwilira mwana wazaka zisanu ndi zitatu.
A Khowaya adapalamula mlanduwu mu shopu yawo imene amayikitsa nyimbo komanso ku tchaja lamya za m’manja.
M’bwalo la milandu, a Khowaya anavomereza kuti ndi olakwa koma anapempha kuti awavere chisoni chifukwa alibe makolo komanso amayang’anira achemwali awo awiri ndi agogo awo.
Koma First Grade Magistrate sanamvere izi ndipo anawagamula kuti apite kundende chifukwa anaphwanya lamulo lomwe lili pa ndime 138.