Bwalo lalikulu la milandu munzinda wa Blantyre likuyembekezeka kupereka chigamulo lero pa mlandu umene anthu ena anakamang’ala kuti bwaloli liwapatse chiletso kuti bungwe la MEC lidzilora anthu kulembetsa mukaundula wa chisankho pogwiritsa ntchito ngakhale chiphaso choyendera komanso chiphaso choyendetsera galimoto.
Oyimira milandu anthuwa, a Felix Tambulasi, anauzanso bwaloli kuti kalata ya chipatala imene anthu amapatsidwa akangobadwa kumene, kalata yochokera kwa a mfumu a m’mudzi umene munthu amachokera, komanso chiphaso cha ukwati ndi njira zina zimene MEC itha kugwiritsa ntchito polemba anthu m’kaundulayu.
Oweruza milandu, a Mandala Mambulasa, ndi amene amve mlanduwu komanso kupereka chigamulo.
Pakadali pano, kalembera wa chisankho cha chaka cha mawa ali mkati m’madera ambiri ndipo bungwe la MEC likugwiritsa ntchito chiphaso cha unzika ngati njira yokhayo yololera anthu kulembetsa.
Olemba: Alufisha Fischer