Kampani ya ku Germany yopanga magetsi a dzuwa ya Sun Power Africa Development yasainira mgwirizano ndi boma la Malawi odzayambitsa ntchito yopanga magetsi okwana 50 megawatts ku Mzuzu ya ndalama zokwana pafupifupi K150 billion.
Nduna ya zamagetsi, a Ibrahim Matola ndi mkulu wa kampaniyi, a Zemo Fleck, ndiwo asainira mgwirizanowu potsiriza pa zokambirana pakati pa Prezidenti Dr Lazarus Chakwera ndi
akuluakulu a ntchito zamalonda ku Germany kudzera ku bungwe la Re Thinking Africa Foundation.
Ntchitoyi aigwira ku Choma ku Mzuzu kudzera ku Mzuzu University.
Ku Germany komweko masiku angapo apitawa, Dr Chakwera akwanitsanso kupeza kampani
zomwe ndi akadaulo a sitima zapamadzi, ndicholinga chakuti
sitima zawo zizidzayenda panyanja ya Malawi pofuna kuthetsa mavuto amayendedwe.