Malawi Broadcasting Corporation
Development Local News Nkhani

Ma Drone awaulutsa

Tindege tating’ono tomwe timajambula zithunzi, drone, atiulutsa m’mwamba ku Bombo kuti tithandizire pa ntchito yosaka ndege yomwe inanyamula wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Dr Saulos Chilima komanso akuluakulu ena asanu ndi anayi.

Malowa ali pansi pa T/A Kabunduli mbali ya m’boma la Nkhatabay komwe kuli nkhalango ya Chikangawa komwe akuganizira kuti ndege yomwe munali Dr Chilima ndi anthu ena, yasowera.

Amene akuulutsa tindegeti ndi a African Drone and Data Academy omwe akuchokera kusukulu ya ukachenjede ya MUST.

Mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, dzulo poyankhula ku mtundu wa a Malawi anapempha nthambi zonse za chitetezo komanso adindo osiyanasiyana kuti atengepo gawo pothandiza pa ntchitoyi mpakana ndegeyi ayipeze.

Olemba: Jackson Sichali

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Government is creating jobs – Chimwendo Banda

MBC Online

SRWB needs K500 million to address flood induced challenge

Earlene Chimoyo

BUSHIRI REACHES OUT TO FOOD INSECURE FAMILIES IN LL RURAL

Madalitso Mhango
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.