Ofalitsankhani kuchipani cha Malawi Congress (MCP), a Jessie Kabwila, apempha anthu m’dziko muno kuti alembetse voti m’madera mwawo pamene ntchitoyi yayamba pofuna kuti chitukuko chimene chipani chawo chikuchita chipitilire.
A Kabwila anena izi Lachisanu masana ku Mitundu m’boma la Lilongwe pamene anayendera nyumba za apolisi mderalo zimene boma likumanga.
Iwo anati masomphenya a chitukuko a 2063 akudalira chitetezo chokhazikika m’magawo a malonda komanso umoyo wa anthu, mwazina.
A Kabwila anati ichi ndi chifukwa chake boma lachilimika poonetsetsa kuti achitetezo m’dziko muno adzikhala malo abwino pomanga nyumbazi m’madera onse adziko lino.
Mfumu Kulera ya mderali yati mafumu ndi okondwa ndipo anathokoza boma chifukwa cha chitukukochi.
M’mbuyomu, boma linalonjeza kuti limanga nyumba za achitetezo a m’dziko muno zokwana K10, 000.