Malawi Broadcasting Corporation
Local Local News Nkhani Politics

Kalembetseni m’kaundula wa MEC kuti mudzavote — MCP

Chipani cha Malawi Congress (MCP) chapempha anthu a mdera la Lilongwe Kumachenga kuti akalembetse mwaunyinji mu kaundula wa bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) kuti adzaponye voti chaka cha mawa.

Mlembi wa mkulu wa MCP, a Richard Chimwendo Banda, anayankhula izi Lamulungu masana pa msonkhano umene chipanichi chinachititsa pabwalo la masewero la Njewa m’boma la Lilongwe.

A Chimwendo Banda anati ndi kofunika kuti anthu mderalo alembetse pamene bungwe la MEC likuyembekezeka kuyamba kalemberayo m’bomalo pa 28 November mpakana pa 11 December chaka chino.

“Prezidenti Dr Lazarus Chakwera akumanga misewu mosakondera, ulimi wa minda ikuluikulu, magetsi anasiya kuvuta, akulimbikitsa ubale wabwino ndi maiko ena ndipo akuika chidwi chotukula miyoyo ya a Malawi. Izitu kuti zipitilire n’kofunika kuti mudzavote,” anatero a Chimwendo Banda.

Pamsonkhanowu, mfumu yaikulu Njewa komanso phungu wa Lilongwe Kumachenga, a Marko Ching’onga, anayamikira boma kaamba ka ntchito za chitukuko zosiyanasiyana zimene akulandira.

Komabe, awiriwa anapempha boma kuti liwamangire msika wa Njewa kuti ochita malonda azitha kugulitsiramo katundu wawo.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

MALAWI SIGNS K26 BILLION PACT WITH AfDB

McDonald Chiwayula

Illovo Sugar launches three-day health camp in CK

Simeon Boyce

Abambo 41 pa 100 sadziwa kuti ali ndi HIV — NAC

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.