Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Immigration ikufuna kukhala ya mphamvu pa masewero

Nthambi ya boma yowona zolowa komanso zotuluka m’dziko muno ya Immigiration yati ikuyika ndondomeko zomwe zichititse kuti akhale ndi ma kalabu komanso osewera omwe adzipikisana nawo komanso kupambana zikho zikuluzikuku za masewero osiyanasiyana a m’dziko muno.

M’modzi mwa ma komishonala a nthambiyi, a Vivian Mwansambo, awuza MBC kuti akufunsa upangiri kuchokera ku nthambi zina za boma monga a polisi komanso MDF kuti aphunzire njira zabwino zopititsira patsogolo masewero awo.

A Kasambo atinso nthambi yawo yakonzeka kugwira ntchito ndi akatswiri omwe si asilikali awo komanso kampani zomwe zili ndi kuthekera kothandiza kukweza masewero wo.

Iwo ati kulemba ntchito osewera omwe ali ndi luso losiyanasiyana ndi njira yokhayo yotukulira masewero ku nthambiyi.

Nthambiyi ili ndi timu ya mpira wa miyendo yomwe ikusewera nawo mu mpikisano wawukulu m’chigawo chakummwera.

 

Olemba Amin Mussa

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

MANEPO yayamikira Madam Chakwera polimbana ndi nkhanza za anthu achikulire

Beatrice Mwape

Malawi deserves easy access to financial investments — RBM

Arthur Chokhotho

NGO drills 500 boreholes in the Southern Region

Jeffrey Chinawa
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.