Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yati ikufuna kuti bungwe la Football Association of Malawi lilowerere pazomwe zinachitika pamasewero awo ndi timu ya MAFCO lamulungu lapitali pabwalo la Kamuzu.
Osewera wa Bullets Wongani Lungu anapondedwa mwadala ndi osewera a MAFCO, Vitumbiko Phiri, Blessings Chandiyang’ana ndi Duncan Mwale m’masewero amu super ligi.
Polankhula ndi atolankhani, presidenti watimuyi, Konrad Buckle wati ndiokhumudwa kwambiri zomwe zinachitikazi ndipo adindo akuyenera abweretse chigamulo chankhaniyi mwansanga.
Lungu akhala pafupifupi sabata imodzi osasewera mpira kamba kakuvulala pamasewerowa.
Mkulu wa Bullets, Albert Chigoga wapemphanso bungwe la oyimbira masewero ampira wa miyendo m’dziko muno kuti aunikilenso zankhaniyi.
Olemba : Praise Majawa