Khothi la Magistrate ku Blantyre lalamula amuna awiri ndi mayi m’modzi kuti apereke chindapusa pa milandu yosiyanasiyana yomwe anapalamula.
Anthuwa ndi a Chifundo Kauwa, 38, a Wongani Mwandira, 41 komanso a Sarah Juwawo a zaka 38.
Ina mwa milandu yomwe anthuwa amawazenga nkuphatikizapo wopezeka ndi makala popanda chilolezo, kuyendetsa galimoto opanda chiphaso choyendetsera komanso kuthawa m’manja mwa achitetezo.
Anthuwa adapalamula milanduyi pa 11 March ndipo galimoto lawo analigwira pa Kameza Roundabout.
Mwa milanduyi, opalamulawa awalamula kulipira chindapusa cha K300,000 komanso K50,000 pa milandu inayo.
M’modzi mwa matekitivi, a Mable Lwanda, atsimikiza za nkhaniyi ponena kuti akugwira limodzi ndi nthambi zosiyanasiyana zaboma pofuna kuthana ndi mchitidwe woononga chilengedwe pootcha makala.
Kusakaza nkhalango pootcha makala ndi zina zomwe zikudzetsa mavuto akusintha kwa nyengo m’dziko muno.