Mlembi wamkulu wa chipani cha UTM a Patricia Kaliati wati malemu Dr Saulos Chilima anaonetsa chitsanzo chabwino potumikira dziko lino modzipereka posayang’ana zigawo.
A Kaliati ayankhula izi ku Mzuzu pa msonkhano wokumbukira malemu Dr Chilima yemwe anali mtsogoleri wa chipani cha UTM komanso wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino.
Iwo ati Dr Chilima anaikapo mtima pofuna kusintha dziko lino komanso kuti achinyamata akhale mzika zodalirika.
Atsogoleri ena a chipani cha UTM anati chipanichi chipitilira kukhala champhamvu pofuna kukwaniritsa masomphenya a yemwe anali mtsogoleri wachipanichi Dr Saulos Chilima.
Dr Chilima pamodzi ndi anthu ena asanu ndi atatu anafa pa ngozi ya ndege ku Chikangawa m’boma la Mzimba pa 10 June 2024.