Katswiri olemba mabuku otchedwa Blessings Chiwosi wati pali zinthu zambiri zomwe dziko la Malawi lingathe kuchita kuti lipite chitsogolo pazachuma komanso chitukuko.
Chiwosi wanena izi pambuyo po kukhazikitsa bukhu lomwe walemba lotchedwa “Malawian wealth creation” lomwe akutambasulamo zinthu zomwe dziko lino likuyenera kuchita kuti likhale lodziyimira palokha.
Mwazina bukhuli lafotokozapo zaulimi komanso nkhani za malonda ndi kuika chidwi pa ntchito zaluso. Iye wati ndizotheka dziko la Malawi kudzichotsa lokha paumphawi koma wati zitengera atsogoleri kugwiritsa ntchito ukadaulo omwe waulemba m’bukuli.
M’mawu ake mkulu wa zamapulani a dziko, a Thomas Munthali ati ndiokondwa kuti achinyamata akuikapo chidwi pokwanitsa masomphenya a dziko. Iwo ati kulemba bukhu logwirizana ndi masomphenyawa ndichitsimikizo choti achinyamata sanatsalire m’mbuyo.