Wapampando wa bungwe loona za chisankho la Malawi Electoral Commission, Justice Annabel Mtalimanja, wati ndi okhutira ndi mmene chisankho chapadera chayendera m’maboma a Mangochi ndi Blantyre.
Iwo ati panalibe mavuto odetsa nkhawa kupatula kuti anthu ena amabwera ndi chaunzika kuti adzavote.
“Pamene tikukonzekera chisankho cha chaka cha mawa, aMalawi akuyenera kudziwa kuti chiphaso cha unzika sichoponyera voti, koma akuyenera kulembetsa kuti adzathe kuponya voti,” iwo anatero.
Chisankho chapaderachi chachitika ku ma Ward a Chilaweni m’boma la Blantyre ndi Mwasa m’boma la Mangochi.
Pakadali pano, ntchito yowerenga mavoti yayamba.
Bungwe la MEC lilengeza zotsatira za chisankhochi mawa pa 24 July 2024 ku Holo ya HHI munzinda wa Blantyre.
Olemba: Secret Segula ndi Arthur Chokhotho