Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Prezidenti Chakwera acheza ndi anthu pa Nanyumbu ku Machinga

Prezidenti Dr Lazarus Chakwera wati zokambirana zimene anali nazo ndi mafumu aku Machinga zayenda bwino.

Dr Chakwera watsimikizira anthu a m’bomali kuti ali ndi chidwi potukula nkhani zaulimi m’dziko muno kuti aliyense adzikhala ndi chakudya chokwanira.

Mtsogoleriyu wayamikira ntchito imene ikuchitika ku scheme ya Mlooka, kumene ulimi wanthilira ukuchitidwa pogwiritsa ntchito mphamvu yadzuwa komanso makina amakono.

Polankhulapo pankhani ya magetsi, Dr Chakwera anati ndi khumbo lake kuti magetsi afikire paliponse mdziko muno, maka mmadera akumidzi.

Potsiliza, mtsogoleri wadziko linoyu walangiza makolo kuti alimbikitse ana awo pankhani ya maphunziro kuti adzakhale odzidalira mtsogolo.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

MANEB lauded for digitalising access to examination results

Chisomo Break

NYCOM splashes K100 million grants for youth

Davie Umar

MEC Commissioner impressed with Balaka

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.