Gawo loyamba la ntchito yomanga chipatala cha makono ku Mponela m’boma la Dowa yatsala pang’ono kutha pomwe pali chiyembekezo kuti anthu adzayamba kulandira thandizo pofika mwezi wa June chaka cha mawa.
Mmodzi wa akulu akulu mu unduna wa za umoyo Dr Sanderson Kuyeli wayankhula izi pomwe adindo a bungwe la National Planning Commission (NPC) komanso Presidential Delivery Unit (PDU) anayendera ntchito yomanga chipatalachi.
A Kuyeli ati ntchito yonse ndi ya ndalama pafupifupi K8 billion, koma m’gawo loyamba analandira K5.7 billion.
Iwo ati pambali pa ndalama yomwe yatsala, apempha unduna wa zachuma kuti uwonjezere ndalama ina yokwana K2 billion kuti amalize ntchito yonse ya mugawo loyamba komanso kugula zipangizo zachipatala kuti adzayambe kuthandiza anthu pofika mwezi wa December.
Ntchito ya mugawo loyamba ndi yomanga maofesi, kolembetsera matenda, malo ochitirako zauchembere wabwino komanso sikelo ya ana, malo oyezera matenda osiyanasiyana komanso komanso kujambulirako ziwalo za mthupiana Out Patients Department (OPD), malo olandilirako mankhwala olimbana ndi kachirombo ka HIV (ARVs) ndikosungirako matupi a omwe atisiya.
Gawo lachiwiri la ntchitoyi yomwenso inayamba kale ndi yomanga malo ogoneka odwala mwazina.
Komishonala wa bungwe la NPC, a Mercy Masoo, amenenso amayimira PDU, anatsindika zakufunika kokweza ntchito zaumoyo m’madera akumidzi, kotero ati ayankhula ndi unduna wa zachuma kuti upereke ndalama kuti ntchito ithe m’mene ayelekezera.
A Masoo atinso mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera akufuna chipatalachi achitsilize msanga kuti anthu a ku Mponela ndi madera ozungulira boma la Dowa, azidzalandira thandizo la za umoyo pafupi.