Chinthuzi: MANA
Mlembi wamkulu wa chipani cha Malawi Congress (MCP), a Richard Chimwendo Banda, ati Prezidenti Dr Lazarus Chakwera ndi chiyembekezo chokhacho cha aMalawi pa nkhani ya chitukuko.
“Prezidenti Chakwera wagwira ntchito zosiyanasiyana monga kumanga misewu ina yomwe idakanika kwa nthawi yaitali, tiyeni tidziyamika,” anatero a Chimwendo Banda.
Iwo anatinso panopa anthu achi alubino akuyenda mosacheukacheuka chifukwa tsopano ali ndi chitetezo chokhwima.
A Chimwendo Banda atsindika kuti chipani chawo chipanga kampeni yabwino yopanda ziwawa ndipo alangiza achinyamata mchipanichi kuti apewe ziwawa.

Wapampando wa MCP mchigawo chapakati, a Zebron Chilondola, ayamika Dr Chakwera chifukwa chodzipereka kukweza dziko lino mu zaka zinayizi ndipo ati iwo adzipereka kugwira ntchito yowonetsetsa kuti Prezidenti Chakwera apambanenso pa chisankhochi.
Poyambilira, Mkulu wa achinyamata mu chipanichi, a Baba Steven Malondera, anayamika boma chifukwa choganizira achinyamata monga kuthandiza sukulu fees ophunzira aku university, omwe tsopano chiwerengero chawo chafika pa 34,000 pamene mmbuyomu anali 10,000 okha.
Iwo analangiza achinyamatawa kuti adzavotere Dr Chakwera pa chisankho chikudzachi.
Nawo a Jean Sendeza, omwe ndi mkulu wa amayi mu chipani cha MCP, alimbikitsa amayi kuti asatengeke ndi atsogoleri otsutsa boma koma akhalebe pambuyo pa Dr Chakwera.
Olemba: Isaac Jali

