Timu ya FCB Nyasa Big Bullets lero ili ndi mdipiti (Street Parade) mumzinda wa Blantyre pomwe, mwazina, akusonyeza zikho zimene timuyi inaanyamula mu season yapitayi.
Malinga ndi mlembi wamkulu wakomiti yamasapota a timuyi, Archibald Kasakura, cholinga chake ndi kuthokoza masapota onse chifukwa choyichemelera timuyi komanso bank ya FCB chifukwa cha thandizo lake.
Ulendowu wayambira pa Kamuzu Upper Stadium kudutsa mu Masauko Chipembere Highway mpaka kukafika mkatikati mwa Blantyre ndipo ukathera ku Ndirande.
#MBCOnlineServices