Bungwe la Green Girls Club lapempha unduna wa za achinyamata kuti uyike njira zoteteza atsikana pa nthawi imene kwagwa ngozi zadzidzidzi, maka zakudza kaamba ka kusintha kwa nyengo.
Poyankhula lero masana ku Lilongwe atagwirana chanza ndi nduna ya achinyamata, a Uchizi Mkandawire, mtsogoleri wa bungweli, Elizabeth Chinga, amene ndi wa zaka 19 zakubadwa,anati panthawiyi atsikana amavutika kwambiri.
Apa panali pa mkumano umene bungwe la UNICEF linachititsa kuti akumane ndi a Mkandawire.
M’mbuyomu, Elizabeth anapulumuka ku namondwe wa Gombe ndi Ana ndipo bungwe la UNICEF linamusankha kukhala m’modzi mwa akazembe a atsikana olimbikitsa ufulu wa atsikana pa nkhani za uchembere wabwino.