Malawi Broadcasting Corporation
Agriculture Development Local Local News

Boma lakhazikitsa ntchito yogawa ufa kwa mabanja omwe akhudzidwa ndi njala

Boma lakhazitsa ntchito yopeleka ufa kwa mabanja omwe akhudzidwa ndi njala yomwe yadza kaamba ka ng’amba yomwe yakhudza maboma ambiri m’dziko muno.

Polankhula pa mwambo okhazikitsa ntchitoyi pa bwalo la sukulu ya Chilangoma ku Chileka mboma la Blantyre, Nduna ya zofalitsa nkhani a Moses Kunkuyu ati boma likudziwa kuti mdziko muno ambiri sakolora chifukwa cha ng’amba.

“Ufa uwu wabwera chifukwa a president was dziko lino Dr Lazarus Chakwera akudziwa kuti mdziko muno muli njala ndipo anenetsa kuti palibe afe ndi njala poti aliyense amene wakhudzidwa ndi njala alandira ufawu” anatero a Kunkuyu.

Pa mwambowu mabanja oposa 1,000 akudera la mfumu yayikulu Kuntaja ndi Kuthembwe ndi omwe alandira mwachiwonetsero.

Ndunayi yadzudzulanso anthu omwe akufalitsa uthenga wabodza oti ufawu siwabwino kudya.

Boma lapeza matumba a ufa okwana matani 23,000 kuti ligawire anthu onse omwe akhudzidwa ndi njala.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

NICE facilitates civic engagement in Dedza

Sothini Ndazi

Chakwera calls for collective effort in the business sector

MBC Online

Kabambe, Mathanga, Mwanamveka, Chiunda appear in court

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.