Timu ya Blue Eagles yalimbikitsa mwayi wake obweleranso mu ligi yaikulu ya TNM pomwe yagonjetsa Ekas Freight Wanderers ndi zigoli zinayi kwa zero pabwalo la Airport Development Limited munzinda wa Lilongwe.
Ganizani James, Laurent Banda, Tonic Vivuyi ndi Miccium Mhone ndiomwe anamwetsa dzigolizi zomwe zapangitsa kuti timuyi idzitsogola ndi mapoinsi 12. Eagles ili ndi ma poyinsi 48 itasewera masewero 18 pomwe Villa yomwe ndiyachiwiri ili ndi ma poyinsi 36 itasewera masewero 17.
Izi zikutanthauza kuti Eagles yomwe siinangonjepo mu ligi ya Chipiku ikungofunika mapoyinsi atatu pamasewero anayi omwe yatsala nawo, Koma mphuzitsi wa timuyi Eliya Kananji wati anyamata ake satayirira chifukwa ulendo wobwelera mu Super League sunatheke.
Zotsatira zamasewero ena omwe aseweredwa lero, Armour Battalion yagonjetsa Wimbe United 3 – 0, St Gabriel Zitha yathambitsa Extreme 3 – 0, pomwe Mitundu Baptist yagonja ndizigoli ziwiri pakhomo ndi timu ya Mbadzi United.