Malawi Broadcasting Corporation
News

Ayamika boma chifukwa cha thandizo la chakudya

Anthu amene akhudzidwa ndi njala ochokera ku ma ward a Matope ndi Malabada ku Ndirande mumzinda wa Blantyre athokoza boma chifukwa chowapatsa thandizo la chakudya.

Anthuwa alankhula izi pa bwalo la za masewero la Kamuzu mumzindawu kumene mabanja oposa 1,000 ochokera ku ma ward awiriwa amalandira matumba achimanga olemera 50 Kg banja lililonse.

Ena mwa anthu amene MBC inayakhula nawo ndi mayi Hawa Tawakali, amene ati ali ndi banja la ana asanu ndi m’modzi ndipo anati thandizoli labwera pa nthawi yoyenera pakuti kunyumba kwawo analibe chakudya chilichonse.

“Polandira chimanga chimenechichi ineyo ndili othokoza kwa mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera chifukwa lero ana anga akatema nsimaz” anatero mayi Tawakali.

Ndipo a Patrick Chirombo amene amakhala ku Makata ku Ndirande ayamika boma chifukwa choganizira anthu a mtawuni amene akhudzidwa ndi njala powapatsa chakudya.

“ Ine ndinalibe chiyembekezo kuti ndipeza chakudya ngati ichi, ineyo ndimalima koma pa ulimi wa chaka chino palibe chomwe ndapeza kuti chikhoza kundithandiza chifukwa cha vuto la ng’amba koma pomwe ndalandira thumba la 50 Kg la chimanga zindithandiza mwinanso kwa miyezi iwiri ku tsogoloku,” a Chirombo afotokoza motero.

Boma lakhazikitsa ntchito zosiyanasiyana pofuna kuthandiza anthu onse amene akhudzidwa ndi njala m’madera akumudzi komanso a mtauni m’dziko muno.

Izi ndikuphatikizapo yopereka ufa okwana matani 23000, kupeleka mtukula pakhomo wa ndalama zokwana K150,000 pa banja komanso kupereka chimanga kwa mabanja omwe akhudzidwa ndi njala kwa miyezi isanu ndi umodzi.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Chakwera arrives at MSG Kanengo Campus

McDonald Chiwayula

MANGOCHI DISTRICT COUNCIL EMBARKS ON A NEW JOURNEY WITH STATE-OF-THE-ART OFFICE COMPLEX

MBC Online

Tobacco market opening shifted to 15 April

Earlene Chimoyo
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.