Malawi Broadcasting Corporation
Local Local News Nkhani Sports Sports

Ndithandiza kutukula mpira kumpoto — Nyasulu

Mmodzi mwa anthu amene akufuna udindo wa wapampando ku bungwe la Northern Region Football Association (NRFA), a Masiya Nyasulu, ati ayika mfundo zokhwima zofuna kusintha masewero a mpira wamiyendo m’chigawo chakumpoto.

A Nyasulu ayankhula izi pamene kwatsala masiku ochepa kuti kuchitike chisankho chosankha adindo oyendetsa masewerowa ku bungweli kuyambira pa 15 February chaka chino.

“Mpira wa dongosolo udziyambira madera akumudzi, kenako kumaboma kuti osewera akamafika posewera ligi yayikulu ya m’chigawochi adzikhala apsya. Kuti izi zitheke, tiyika ndalama m’maboma onse zothandizira dongosolo limeneli,” iwo anatero.

Iwo anaonjezera kuti masomphenya awo akugwirizana ndi mfundo zimene bungwe la Football Association of Malawi likunena lofuna kutukula masewerowa m’dziko muno.

A Nyasulu akupikisana ndi amene akugwirizira panopa ngati wapampando, a Chauka Mwasinga.

Kumsonkhano waukulu wa bungweli, anthu osiyanasiyana akasankhanso mlembi wamkulu, msungichuma komanso mamembala a komiti yayikulu atsopano.

Olemba: Hassan Phiri

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

School Leadership Program can improve students’ performance — Education Ministry

MBC Online

British Govt reaffirms support for meteorological services

Charles Pensulo

NFRA to start maize procurement on May 13

error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.